Chiyanjano

Chiyanjano chimatanthauza kubwera pamodzi ndi Akhristu ena omwe akukhala moyo wofanana ndi inu. Kumaphatikizapo kulimbikitsana ndi umodzi mu cholinga ndi mzimu umene umafika mozama kwambiri kuposa ubwenzi kapena maunansi a anthu. ( 1 Yoh. 1:7 ) Timapezanso chiyanjano ndi Khristu pamene tigonjetsa uchimo m’nthawi ya mayesero monga mmene anachitira pamene anali munthu. Mwanjira imeneyi timam’dziŵa bwino ndipo timakhala paubale ndi umodzi ndi Iye. ( Afilipi 3:10 )